1 Nʼchifukwa chake, ife tiyenera kusamalira kwambiri zimene tinamva, kuopa kuti pangʼono ndi pangʼono tingazitaye. 2 Popeza uthenga umene unayankhulidwa kudzera mwa angelo unali okhazikika ndithu, choncho aliyense amene ananyozera ndi kusamvera analandira chilango choyenera. 3 Nanga ife tidzapulumuka bwanji tikapanda kusamala chipulumutso chachikulu chotere? Ambuye ndiye anayamba kuyankhula za chipulumutsochi, kenaka amenenso anamvawo anatitsimikizira. 4 Mulungu anachitiranso umboni pochita zizindikiro, zinthu zodabwitsa ndi zamphamvu zamitundumitundu ndi powapatsa mphatso za Mzimu Woyera monga mwachifuniro chake.
5 Mulungu sanapereke kwa angelo ulamuliro wa dziko limene likubwerali, limene ife tikulinena. 6 Koma palipo pena pamene wina anachitira umboni kuti,
10 Mulungu amene analenga zinthu zonse ndipo zinthu zonse zilipo chifukwa cha Iye ndi mwa Iye, anachiona choyenera kubweretsa ana ake ambiri mu ulemerero. Kunali koyenera kudzera mʼnjira ya zowawa, kumusandutsa Yesu mtsogoleri wangwiro, woyenera kubweretsa chipulumutso chawo. 11 Popeza iye amene ayeretsa ndi oyeresedwa onse ndi abanja limodzi. Nʼchifukwa chake Yesu sachita manyazi kuwatcha iwo abale ake. 12 Iye akuti,
14 Tsono popeza kuti anawo ndi anthu, okhala ndi mnofu ndi magazi, Yesu nayenso anakhala munthu ngati iwowo kuti kudzera mu imfa yake awononge Satana amene ali ndi mphamvu yodzetsa imfa. 15 Pakuti ndi njira yokhayi imene Iye angamasule amene pa moyo wawo wonse anali ngati akapolo chifukwa choopa imfa. 16 Pakuti tikudziwanso kuti sathandiza angelo, koma zidzukulu za Abrahamu. 17 Chifukwa cha zimenezi, Iye anayenera kukhala wofanana ndi abale ake pa zonse, kuti akhale mkulu wa ansembe wachifundo ndi wokhulupirika potumikira Mulungu, kuti potero achotse machimo a anthu. 18 Popeza Iye mwini anamva zowawa pamene anayesedwa, Iyeyo angathe kuthandiza amene akuyesedwanso.
<- AHEBRI 1AHEBRI 3 ->