1 Nthawi inanso analowa mʼsunagoge, ndipo munthu wa dzanja lolumala anali momwemo. 2 Ena a iwo anafunafuna chifukwa chakuti akamuneneze Yesu, potero anamuyangʼanitsitsa kuti aone ngati angamuchiritse tsiku la Sabata. 3 Yesu anati kwa munthu wolumala dzanjayo,
4 Ndipo Yesu anawafunsa kuti,
5 Yesu anawayangʼana ndi mkwiyo ndipo powawidwa mtima chifukwa cha mitima yawo yowuma anati kwa munthuyo,
7 Yesu anachoka pamodzi ndi ophunzira ake napita ku nyanja, ndipo gulu lalikulu la anthu lochokera ku Galileya linamutsata. 8 Atamva zonse zimene amachita, anthu ambiri anabwera kwa Iye kuchokera ku Yudeya, Yerusalemu, Idumeya ndi madera a ku tsidya kwa mtsinje wa Yorodani ndi ozungulira Turo ndi Sidoni. 9 Chifukwa cha gulu la anthu, anawuza ophunzira ake kuti apezeretu bwato likhale, kuti anthu angamupanikize. 10 Pakuti anachiritsa ambiri, kotero kuti iwo amene anali ndi matenda amakankhana kutsogolo kuti amukhudze. 11 Nthawi iliyonse mizimu yoyipa ikamuona, imagwa pansi pamaso pake ndi kufuwula kuti, “Inu ndinu Mwana wa Mulungu!” 12 Koma anayichenjeza mwamphamvu kuti isanene kuti Iye anali ndani.
13 Yesu anakwera ku phiri ndipo anayitana amene anawafuna, ndipo anabwera kwa Iye. 14 Iye anasankha khumi ndi awiri, nawayika akhale atumwi; pokhala ndi Iye aziwatuma kukalalikira 15 ndi kuti akhale ndi ulamuliro wotulutsa ziwanda. 16 Awa ndi khumi ndi awiri amene anawasankha: Simoni (amene anapatsidwa dzina lakuti Petro); 17 Yakobo mwana wa Zebedayo, ndi mʼbale wake Yohane (iwowa anawapatsa dzina lakuti Bowanege, ndiye kuti ana a bingu); 18 Andreya, Filipo, Bartumeyu, Mateyu, Tomasi, Yakobo mwana wa Alufeyo, Tadeyo, Simoni Zelote, 19 ndi Yudasi Isikarioti, amene anamupereka Iye.
20 Pambuyo pake Yesu analowa mʼnyumba, ndipo gulu la anthu linasonkhananso, kotero kuti Iye pamodzi ndi ophunzira ake sanapeze mpata kuti adye. 21 Anthu a ku banja lake atamva zimenezi, anapita kuti akamutenga, pakuti ankanena kuti, “Wazungulira mutu.”
22 Ndipo aphunzitsi amalamulo omwe anachokera ku Yerusalemu anati, “Iye wagwidwa ndi Belezebabu! Ndi ulamuliro wa mkulu wa ziwanda akutulutsa ziwanda.”
23 Pamenepo Yesu anawayitana nawayankhula mʼmafanizo nati:
30 Ananena izi chifukwa anati, “Ali ndi mzimu woyipa.”
31 Pamenepo amayi ndi abale ake a Yesu anafika. Atayima kunja, anatuma wina kuti akamuyitane Iye. 32 Gulu la anthu linakhala momuzungulira Iye, ndipo anamuwuza kuti, “Amayi ndi abale anu ali panja akukufunani.”
33 Iye anafunsa kuti,
34 Pamenepo anayangʼana anthu amene anakhala momuzungurira ndipo anati,