1 Ndipo anawawuza kuti, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti ena amene ayimirira pano sadzafa asanaone ufumu wa Mulungu ukubwera mwa mphamvu.”
Maonekedwe a Ulemerero wa Yesu pa Phiri
2 Patatha masiku asanu ndi limodzi Yesu anatenga Petro, Yakobo ndi Yohane nawatsogolera kupita ku phiri lalitali, kumene anali okhaokha. Kumeneko maonekedwe ake anasinthika pamaso pawo. 3 Zovala zake zinawala monyezimira kwambiri, kotero kuti palibe sopo wina aliyense amene angaziyeretse monyezimira chotere pa dziko la pansi. 4 Ndipo anaonekera Eliya ndi Mose pamaso pawo, amene ankayankhulana ndi Yesu.
5 Petro anati kwa Yesu, “Aphunzitsi, ndi kwabwino kuti ife tili pano. Tiyeni timange misasa itatu; umodzi wanu, wina wa Mose ndi wina wa Eliya.” 6 (Iye sanadziwe choti anene, anali ndi mantha akulu).
7 Pamenepo mtambo unaoneka ndi kuwaphimba, ndipo mawu anamveka kuchokera mu mtambo kuti, “Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa. Mvereni Iye!”
8 Mwadzidzidzi, atayangʼanayangʼana, sanaonenso wina aliyense ali ndi iwo kupatula Yesu.
9 Pamene ankatsika kuchokera ku phiri, Yesu anawalamulira kuti asawuze aliyense zimene anaona mpaka Mwana wa Munthu atauka kwa akufa. 10 Iwo anayisunga nkhaniyo nakambirana za tanthauzo lake la “Kuuka kwa akufa.”
25 Yesu ataona kuti gulu la anthu likuthamangira kumalowo, anadzudzula mzimu woyipawo kuti, “Iwe mzimu wolepheretsa kuyankhula ndi kumva, ndikulamulira tuluka mwa iye ndipo usadzalowenso.”
26 Mzimuwo unafuwula ndi kumugubuduza kwambiri ndipo unatuluka. Mnyamatayo anaoneka ngati mtembo ndipo ambiri anati, “Wafa.” 27 Koma Yesu anamugwira dzanja ndipo anamuyimiritsa, ndipo anayimirira.
28 Yesu atalowa mʼnyumba, ophunzira ake anamufunsa ali pa okha kuti, “Kodi ndi chifukwa chiyani ife sitinathe kutulutsa chiwandacho?”
29 Iye anayankha kuti, “Mtundu uwu umatuluka pokhapokha mwapemphera ndi kusala kudya.”
Yesu aneneratu za Imfa yake Kachiwiri
30 Anachoka malo amenewo nadutsa ku Galileya. Yesu sanafune kuti wina aliyense adziwe kumene anali, 31 chifukwa amaphunzitsa ophunzira ake. Anati kwa iwo, “Mwana wa Munthu adzaperekedwa mʼmanja mwa anthu. Adzamupha, ndipo patatha masiku atatu adzauka.”32 Koma sanazindikire chimene amatanthauza, ndipo anachita mantha kuti amufunse.
Wamkulu Ndani mu Ufumu wa Mulungu?
33 Anafika ku Kaperenawo. Pamene anali mʼnyumba, anawafunsa kuti, “Kodi mumatsutsana chiyani mʼnjira muja?”34 Koma anakhala chete chifukwa ali mʼnjira amatsutsana za kuti wamkulu kuposa onse ndani.
35 Atakhala pansi, Yesu anayitana khumi ndi awiriwo nati, “Ngati wina aliyense afuna kukhala woyamba, ayenera kukhala wotsiriza ndi wotumikira onse.”
36 Anatenga kamwana nakayimiritsa pakati pawo ndipo anawawuza kuti, 37“Aliyense wolandira mmodzi wa ana angʼono awa mʼdzina langa alandira Ine; ndipo aliyense wolandira Ine salandira Ine koma amene anandituma.”
39 Yesu anati, “Musamuletse, palibe amene amachita chodabwitsa mʼdzina langa ndipo kenaka nanena zoyipa za Ine,40pakuti aliyense amene satsutsana nafe ali mbali yathu.41Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti aliyense amene akupatsani chikho cha madzi mʼdzina langa chifukwa ndinu ake a Khristu, sadzataya konse mphotho yake.”
Zochimwitsa Ena
42“Ndipo ngati wina aliyense achimwitsa mmodzi wa ana angʼono awa amene akhulupirira Ine, kukanakhala bwino kwa iye kuti aponyedwe mʼnyanja atamangiriridwa mwala waukulu mʼkhosi mwake.43Ngati dzanja lako likuchimwitsa, lidule. Ndi kwabwino kwa iwe kulowa mʼmoyo ndi dzanja limodzi kusiyana ndi kukhala ndi manja awiri ndi kupita ku gehena, kumene moto wake suzima.44(Kumene mphutsi zake sizifa ndipo moto wake suzima).45Ndipo ngati phazi lako likuchimwitsa, lidule. Ndi kwabwino kwa iwe kulowa mʼmoyo olumala kusiyana ndi kukhala ndi mapazi awiri ndi kuponyedwa mu gehena.46(Kumene mphutsi zake sizifa ndipo moto wake suzima).47Ndipo ngati diso lako likuchimwitsa, likolowole. Ndi kwabwino kwa iwe kulowa ufumu wa Mulungu ndi diso limodzi, kusiyana ndi kukhala ndi maso awiri ndi kuponyedwa mu gehena,48kumene
“ ‘mphutsi zake sizifa
ndipo moto wake suzima.’
49Aliyense adzayesedwa ndi moto.
50“Mchere ndi wabwino, koma ngati utasukuluka, mungawukoleretsenso bwanji? Mukhale nawo mchere mwa inu nokha, ndipo mukhale pa mtendere wina ndi mnzake.”